Ukadadziwa zobisala mtimamu
Nyimbo zosaimbidwa zogonera mbongomu
Mawu okoma oba mphasa mmilomomu
Ntchito zogometsa zochita akangaude mmanjamu
Zithunzi zobisika mmasomu
Mapulani a zakazaka odikhana bwino mmutumu
Chimwemwe chadzala mtsayamu
Ndawala zochititsa dzanzi mmiyendomu
Chikondi chosefukira chili pa liwiro mmitsemphamu
Bata lopezeka mthupimu
Ukadadziwa zonenedwa mndakatuloyi

Ukadakumbukira zokambidwa pa dzana
Sibwenzi lero tili mbiri chabe
Ukadalota zodza mawa
Bwezi lero utandipatsa chanza
Ukadadziwa zokhumba zanga
Ukadati bwera ukhale wanga
Ukadafunsa mwina
Bwezi pano zitafumbira
Ukadanvetsera
Nkupenyetsetsa
Ukadadziwa

Leave a comment

Trending

Design a site like this with WordPress.com
Get started