Latest
-

Ukadadziwa
Ukadadziwa zobisala mtimamu Nyimbo zosaimbidwa zogonera mbongomu Mawu okoma oba mphasa mmilomomu Ntchito zogometsa zochita akangaude mmanjamu Zithunzi zobisika mmasomu Mapulani a zakazaka odikhana bwino mmutumu Chimwemwe chadzala mtsayamu Ndawala zochititsa dzanzi mmiyendomu Chikondi chosefukira chili pa liwiro mmitsemphamu Bata lopezeka mthupimu Ukadadziwa zonenedwa mndakatuloyi



